Bible ReaderKumwalira kwa Yosefe

1Ndipo Yosefe anagwapa nkhope ya atate wace, namlirira iye nampsompsona iye. 2Ndipo Yosefe anauza akapolo ace asing'anga kutiakonze atate wace: ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israyeli. 3Ndipo anatha masiku ace makumi anai a iye; cifukwa comweco amatsiriza masiku akukonza thupi; ndipo Aaigupto anamlira iye masiki makumi asanu ndi awiri.

4Atapita masiku akumlira iye Yosefe anati kwa mbumba ya Farao kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamase panu, nenanitu m'makutu a Parae kuti, 5Atate wanga anandilumbi ritsa ine, kuti, Taona, ndirinkufa m'manda m'mene ndadzikonzeran ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundi loletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabwe ranso. 6Ndipo Farao anati, Pita kaike atate wako, monga iye anaku lumbiritsa iwe. 7Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wace; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akuru a pa mbumba yace, ndi akuru onse a m'dziko la Aigupto, 8ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ace, ndi mbumba ya atate wace: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni. 9Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magareta ndi apakavalo; ndipo panali khamc lalikuru. 10Ndipo anafika pa dwale la Atadi, liri tsidya lija la Yordano, pamenepo anamlira maliro a atate wace masiku asanu ndi limodzi. 11Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo; Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro akuru a Aaigupto: cifukwa cace dzina la pamenepo linachedwa Abeli-mizraimu, pali tsidya lija la Yordano. 12Ndipo ana ace amuna anamcitira iye monga anawalamulira iwo; 13cifukwa kuti ana ace amuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pace, kwa Efroni Mhiti, patsogolo pa Mamre.

14Ndipo ataika atate wace, Yosefe mabwera ku Aigupto, iye ndi abale ace, ndi onse amene anakwera pamodzi naye kukaika atate wace. 15Ndipo pamene abale ace a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamcitira iye. 16Ndipo anatumiza mthenga kwa Yosefe kuti, Atate wathu asanafe analamulira, kuti, 17Muziti cotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kucimwa kwao, cifukwa kuti anakucitirani inu coipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa aka polo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye. 18Ndiponso abale ace anamuka namgwadira pamaso pace; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu. 19Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndiri ine kodi m'malo a Mulungu? 20Koma inu, munandipangira ine coipa; koma Mulungu anacipangira cabwino, kuti kucitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri, 21Ndipo tsopano musaope; Ine ndidzacereza inu, ndi ana anu ang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.

22Ndipo Yosefe anakhala m'Aigupto, iye, ndi mbumba ya atate wace; ndipo Yosefe anakhala ndi movo zaka zana limodzi ndi khumi. 23Ndipo Yosefe anaona ana a Efraimu a mbadwo wacitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe. 24Yosefe ndipo anati kwa abale ace, Ndirinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakucotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isake, ndi kwa Yakobo 25Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israyeli kuti, Mulungu adzaonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nao mafupa anga kucokera kuno. 26Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lace ndi mankhwala osungira, ndipo ariamuika iye m'bokosi m'Aigupto.